Judges 17:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mika atabweza ndalamazo kwa mai wake, mai wakeyo adatengapo ndalama zasiliva 200 nazipereka kwa mmisiri wosula siliva. Munthuyo adasema fano nasungunula ndalamazo, nakutira fanolo ndi siliva. Ndipo Mika adaliimika m'nyumba mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anambwezera mai wake ndalamazo, mai wake anatapako ndalama mazana awiri, nazipereka kwa woyenga, ndiye anazipanga fano losema ndi fano loyenga; ndipo linakhala m'nyumba ya Mika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mika atabweza ndalama zija kwa amayi ake, iwo anatengapo ndalama za siliva 200 namupatsa mmisiri wosula siliva. Iye anakonza fano, nasungunula siliva uja ndi kulikutira fano lija. Ndipo Mika anayika fanolo mʼnyumba mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anambwezera mai wace ndaramazo, mai wace anatapako ndarama mazana awiri, nazipereka kwa woyenga, ndiye anazipanga fane losema ndi fano loyenga; ndipo linakhala m'nyumba ya Mika.