Judges 17:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mikayo anali ndi kachisi wakewake, ndipo adapanga chovala chaunsembe cha efodi ndiponso mafano am'nyumba otchedwa terafimu, nakhazika mmodzi mwa ana ake kuti akhale wansembe wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma munthuyu Mika anali nayo nyumba ya milungu, napanga chovala cha wansembe, ndi timafano, namninkha zansembe mwana wake wina wamwamuna, amene anakhala wansembe wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mikayu anali ndi kachisi, ndipo anapanga efodi ndi mafano otchedwa terafimu. Anapatula mwana wake mmodzi kuti akhale wansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma munthuyu Mika anali nayo nyumba ya milungu, napanga cobvala ca wansembe, ndi timafano, namninkha zansembe mwana wace wina wamwamuna, amene anakhala wansembe wace.