Judges 17:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo adachoka ku mudzi wa Betelehemu uja ku Yuda, kukafunafuna kwina kokakhala. Akuyenda ulendo wakewo adakafika ku dziko lamapiri la ku Efuremu ku nyumba ya Mika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adachokera munthuyo m'mudzi m'Betelehemu-Yuda, kugonera paliponse akapeza pokhala; ndi pa ulendo wake anafika ku mapiri a Efuremu, kunyumba ya Mika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyeyu anachoka mu mzinda wa Betelehemu uja ku Yuda kukafuna malo ena okhala. Akuyenda, anafika ku dziko la mapiri la Efereimu ku nyumba ya Mika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adacokera munthuyo m'mudzi m'Betelehemu-Yuda, kugonera pali ponse akapeza pokhala; ndi pa ulendo wace anafika ku mapiri a Efraimu, ku nyumba ya Mika.