Judges 18:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo kunalibe mfumu ku dziko la Israele. Anthu a fuko la Dani ankafunafuna dziko loti azikhalamo, kuti likhale choloŵa chao, pakuti mpaka nthaŵi imeneyo nkuti iwowo asanalandire choloŵa pakati pa mafuko a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku ajawo panalibe mfumu m'Israele; masiku ajanso fuko la Adani anadzifunira cholowa chakukhalako; pakuti kufikira tsiku lija sichinawagwera cholowa chao pakati pa mafuko a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masiku amenewo munalibe mfumu mu Israeli. Ndipo anthu a fuko la Dani amafunafuna malo okhalamo ngati cholowa chawo, chifukwa kufikira nthawi imeneyo anali asanalandire cholowa chawo pakati pa mafuko a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku ajawo panalibe mfumu m'Israyeli; masiku ajanso pfuko la Adani anadzifunira colowa cakukhalako; pakuti kufikira tsiku lija sicinawagwera colowa cao pakati pa mapfuko a Israyeli.