Judges 18:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adakamanga zithando zankhondo ku Kiriyati-Yearimu m'dziko la Yuda. Chifukwa cha chimenechi malowo akutchedwa zithando za Dani mpaka pano, ndipo ali kuzambwe kwa Kiriyati-Yearimu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nakwera namanga misasa m'Kiriyati-Yearimu, m'Yuda; chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo chigono cha Dani, mpaka lero; taona, ali m'tseri mwa Kiriyati-Yearimu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anakamanga msasa ku Kiriati-Yearimu mʼdziko la Yuda. Malowa ali kumadzulo kwa Kiriati-Yearimu. Ichi ndi chifukwa chake malowo akutchedwa Mahane Dani mpaka lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nakwera namanga misasa m'Kiriyati-yearimu, m'Yuda; cifukwa cace anacha dzina lace la malowo cigono ca Dani, mpaka lero; taona, ali m'tseri mwa Kiriyatiyearimu.