Judges 18:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu asanu amene adaapita kukazonda dziko la Laisi aja adaŵafunsa abale aowo kuti, “Kodi mukudziŵa kuti imodzi mwa nyumba zimenezi muli chovala cha efodi, mafano am'nyumba, otchedwa terafimu, ndiponso fano losema ndi lina lachitsulo? Ndiye mudziŵa chochita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anayankha amuna asanu anamukawo kukazonda dziko la Laisi, nanena ndi abale ao, Kodi mudziwa kuti m'nyumba izi muli chovala cha wansembe, ndi timafano ndi fano losema, ndi fano lonyenga? Ndipo tsopano dziwani choyenera inu kuchita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu asanu amene anakazonda dziko la Laisi anati kwa abale awo, “Kodi mukudziwa kuti imodzi mwa nyumba izi muli efodi, mafano a mʼnyumba otchedwa terafimu, fano losema ndiponso fano lokuta ndi siliva? Ndiye mudziwe chochita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anayankha amuna asanu anamukawo kukazonda dziko la Laisi, nanena ndi abale ao, Kodi mudziwa kuti m'nyumba izi muli cobvala ca wansembe, ndi timafano ndi fano losema, ndi fano loyenga? Ndipo tsopano dziwani coyenera inu kucita.