Judges 18:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adapatuka nakafika kunyumba kwa Mika, kumene mnyamata wachilevi uja ankakhala, nakamufunsa m'mene zinkamuyendera zinthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napatuka iwo kumkako, nafika kunyumba ya mnyamata Mleviyo, ndiyo nyumba ya Mika, namfunsa ngati ali bwanji.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthuwa anapatuka napita ku nyumba ya Mika kumene mnyamata, Mlevi uja ankakhala ndipo anamufunsa za mmene zinthu zilili.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napambuka iwo kumkako, nafika ku nyumba ya mnyamata Mleviyo, ndiyo nyumba ya Mika, namfunsa ngati ali bwanji.