Judges 18:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo anthu asanu amene adaali atazonda dziko aja adakaloŵa nakatenga fano losema lija, chovala cha efodi, mafano am'nyumba aja, ndi fano lachitsulo. M'menemo nkuti wansembe ataimirira pa khomo lapachipata pamodzi ndi anthu 600 okhala ndi zida zankhondo aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma amuna asanu omukawo kukazonda dziko anakwera analowako, natenga fano losema, ndi chovala cha wansembe ndi timafano, ndi fano loyenga; ndi wansembe anaima polowera pa chipata pamodzi ndi amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida za nkhondo m'chuuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu asanu amene anakazonda dziko aja analowa ndi kukatenga fano losema, efodi, fano la mʼnyumba lotchedwa terafimu, ndi fano lokutidwa ndi siliva. Nthawiyi nʼkuti wansembe uja ndi anthu 600 okhala ndi zida za nkhondo aja ali chiyimire pa chipata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma amuna asanu omukawo kukazonda dziko anakwera nalowako, natenga fano losema, ndi cobvala ca wansembe ndi timafano, ndi fano loyenga; ndi wansembe anaima polowera pa cipata pamodzi ndi amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida za nkhondo m'cuuno.