Judges 18:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adamuyankha kuti, “Khala chete, usalankhule, tiye kuno, ukakhale mlangizi wathu ndi wansembe wathu. Kodi si kwabwino koposa kwa iwe kuti ukhale wansembe wa fuko lathunthu la Israele m'malo mokhala wansembe wa munthu mmodzi yekha?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena naye, Khala chete, tseka pakamwa pako, numuke nafe, nutikhalire atate ndi wansembe wathu; chikukomera nchiti, kukhala wansembe wa nyumba ya munthu mmodzi, kapena kukhala wansembe wa fuko ndi banja m'Israele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anamuyankha kuti, “Khala chete usayankhule. Tsagana nafe ndipo udzakhala mlangizi wathu ndi wansembe wathu. Kodi si kwabwino kwa iwe kukhala wansembe wa fuko lonse la Israeli mʼmalo mokhala wansembe wa munthu mmodzi yekha?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena naye, Khala cete, tseka pakamwa pako, numuke nafe, nutikhalire atate ndi wansembe wathu; cikukomera nciti, kukhala wansembe wa nyumba ya munthu mmodzi, kapena kukhala wansembe wa pfuko ndi banja m'Israyeli?