Judges 18:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho anthu a fuko la Daniwo adatuma anthu asanu olimba mtima, osankhidwa mwa mabanja ao onse. Anthuwo adachokera ku Zora ndi ku Esitaoli, adatumidwa kuti akazonde dziko ndi kuliyendera. Anthu onse adaŵauza kuti, “Pitani mukayendere dzikolo.” Iwowo adakafika ku dziko lamapiri la ku Efuremu ku nyumba ya Mika, nagona komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Dani anatuma a banja lao amuna asanu a mwa iwo onse, anthu olimba mtima, a ku Zora, ndi a ku Esitaoli, kuzonda dziko ndi kufunafunamo; nanena nao, Mukani, mufunefune m'dziko. Nafika iwo ku mapiri a Efuremu kunyumba ya Mika, nagona komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho fuko la Dani linatumiza kuchokera ku mabanja awo onse anthu olimba mtima asanu. Anthuwa anachokera ku Zora ndi ku Esitaoli ndipo anatumidwa kukazonda ndi kuliyendera dzikolo. Anthu amenewa ankayimira fuko lonse la Dani. Anthuwa anawawuza kuti, “Pitani mukazonde dzikolo.” Anthuwa anafika ku dziko la mapiri la Efereimu ndi kupita ku nyumba ya Mika komwe anakagona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Dani anatuma a banja lao amuna asanu a mwa iwo onse, anthu olimba mtima, a ku Zora, ndi a ku Esitaoli, a kuzonda dziko ndi kufunafunamo; nanena nao, Mukani, mufunefune m'dziko. Nafika iwo ku mapiri a Efraimu ku nyumba ya Mika, nagona komweko,