Judges 18:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mtima wake wa wansembeyo udasangalala, ndipo adatenga chovala cha efodi, mafano am'nyumba, ndi fano losema lija, natsagana nawo anthuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nukondwera mtima wa wansembeyo, natenga iye chovala cha wansembe, ndi timafano ndi fano losema, nalowa pakati pa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembeyo anakondwera ndipo anatenga efodi, fano la mʼnyumba ndi fano losema natsagana nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nukondwera mtima wa wansembeyo, natenga iye cobvala ca wansembe, ndi timafano ndi fano losema, nalowa pakati pa anthu.