Judges 18:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atapita kamtunda ndithu kuchokera pa nyumba ya Mika, Mikayo ndi anthu amene anali m'nyumba zoyandikana naye, adasonkhana kuti alondole anthu a fuko la Dani ndipo adaŵapeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atafika kutali ndi nyumba ya Mika, Mikayo anawamemeza amuna a m'nyumba zoyandikizana ndi yake, natsata ndi kuwapeza ana a Dani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atayenda mtunda pangʼono kuchokera pa nyumba ya Mika, anthu amene amakhala pafupi ndi nyumba ya Mika anasonkhana kulondola a fuko la Dani aja, ndipo anawapeza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atafika kutari ndi nyumba ya Mika, Mikayo anawamemeza amuna a m'nyumba zoyandikizana ndi yace, natsata ndi kuwapeza ana a Dani.