Judges 18:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mika adaŵayankha kuti, “Mwanditengera milungu yanga imene ine ndidapanga, mwandilandanso wansembe wanga nkumapita, nanga ine chanditsalira nchiyani? Ndiye inu mungandifunse kuti, ‘Kodi chakuvuta nchiyani?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Mwanditengera milungu yanga ndinaipanga, ndi wansembe, ndi kuchoka; chinditsaliranso chiyani? Ndipo muneneranji kwa ine, Chakusowa nchiyani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Inu mwanditengera milungu imene ndinapanga pamodzi ndi wansembe nʼkumapita. Tsono ine ndatsala ndi chiyani? Ndiye inu mungafunse kuti chavuta nʼchiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Mwanditengera milungu yanga ndinaipanga, ndi wansembe, ndi kucoka; cinditsaliranso ciani? ndipo muneneranji kwa ine, Cakusowa nciani?