Judges 18:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a fuko la Dani aja adayankha kuti, “Usaonjezenso mau ena, mwinamwina anthu aŵa apsa mtima nakumenya, ndipo iweyo ndi banja lako nonse muphedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ana a Dani anati kwa iye, Mau ako asamveke ndi ife, angakugwere anthu owawa mtima, nukataya moyo wako ndi wa iwo a m'nyumba mwako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a fuko la Dani aja anayankha kuti, “Usayankhuleponso kanthu chifukwa anthu awa angapse mtima nakumenya ndipo iwe ndi banja lako lonse nʼkutayapo miyoyo yanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ana a Dani anati kwa iye, Mau ako asamveke ndi ife, angakugwere anthu owawa mtima, nukataya moyo wako ndi wa iwo a m'nyumba mwako.