Judges 18:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatenga zinthu zimene Mika adapanga zija pamodzi ndi wansembe wake uja, anthu a fuko la Daniwo adakafika ku Laisi kwa anthu aphee ndi opanda tcheru aja. Adaŵathira nkhondo naŵapha, nkutentha mzinda wao ndi moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo anatenga zimene Mika adachipanga, ndi wansembe anali naye, nafika ku Laisi, kwa anthu odekha ndi okhazikika mtima, nawakantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi wao ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a fuko la Dani aja anatenga zinthu zimene Mika anapanga pamodzi ndi wansembe uja. Iwo anakafika ku Laisi kwa anthu a phee, osatekeseka aja ndipo anawathira nkhondo, nawapha ndi kutentha mzindawo ndi moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo anatenga zimene Mika adacipanga, ndi wansembe anali naye, nafika ku Laisi, kwa anthu odekha ndi okhazikika mtima, nawakantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi wao ndi moto.