Judges 18:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunalibe oŵapulumutsa, popeza kuti kunali kutali ndi ku Sidoni ndipo sankayenderana konse ndi anthu ena. Mzindawo unali m'chigwa cha ku Beterehobu. Anthu a fuko la Daniwo adamanganso mzindawo ndi kumakhalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panalibe wolanditsa, popeza ku Sidoni nkutali, ndipo analibe kuyenderana ndi anthu ena; ndiko ku chigwa chokhala ku Beterehobu. Pamenepo anamanganso mudziwo, nakhala m'mwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panalibe wowapulumutsa chifukwa anali kutali ndi Sidoni ndiponso sanali pa ubale ndi wina aliyense. Mzindawo unali mʼchigwa cha Beti-Rehobu. Anthu a fuko la Adaniwo anawumanganso mzindawo ndi kumakhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panalibe wolanditsa, popeza ku Sidoni nkutali, ndipo analibe kuyenderana ndi anthu ena; ndiko ku cigwa cokhala ku Betirehobo. Pamenepo anamanganso mudziwo, nakhala m'mwemo.