Judges 18:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzindawo adautcha Dani kutengera dzina la Dani kholo lao, amene anali mwana wa Israele. Koma dzina la mzindawo poyamba lidaali Laisi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analitcha dzina la mudziwo Dani, kutsata dzina la atate wao Dani wombala Israele; koma poyambapo dzina la mudzi linali Laisi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anawutcha mzindawo Dani, kutengera dzina la kholo lawo Dani, amene anali mwana wa Israeli, ngakhale kuti mzindawo poyamba unali Laisi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analicha dzina la mudziwo Dani, kutsata dzina la atate wao Dani wombala Israyeli; koma poyambapo dzina la mudzi linali Laisi.