Judges 18:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu a fuko la Dani aja adaimiritsa fano la siliva wosungunula lija. Ndipo Yonatani, mwana wa Geresomo, mwana wa Mose, pamodzi ndi ana ake onse, adakhala ansembe a anthu a fuko la Dani mpaka pa tsiku la ukapolo wa dzikolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Dani anadziimitsira fano losemalo; ndi Yonatani mwana wa Geresomo mwana wa Manase, iye ndi ana ake amuna anali ansembe a fuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a fuko la Dani anayimiritsa fano losema lija. Yonatani mwana wa Geresomu, mwana wa Mose pamodzi ndi ana ake onse anakhala ansembe a fuko la Dani mpaka pa tsiku la ukapolo wa dzikolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Dani anadziimitsira fane losemalo; ndi Yonatani mwana wa Gerisomu mwana wa Manase, iye ndi ana ace amuna anali ansembe a pfuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko.