Judges 18:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo anthu asanu aja adachoka nakafika ku Laisi. Adakaona anthu amene ankakhala kumeneko, nazindikira kuti anthuwo ankakhala popanda choŵavuta, monga momwe ankakhalira Asidoni. Anali anthu aphee ndi opanda tcheru, osasoŵa kanthu kalikonse ndiponso anali anthu achuma. Adaona kuti anthuwo ankakhala kutali ndi Asidoni ndipo sankayenderana konse ndi anthu ena.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo amuna asanuwa anachoka, nafika ku Laisi; naona anthu anali m'mwemo, kuti anakhala okhazikika mtima, monga anakhala Asidoni, odekha ndi osatekeseka; popeza m'dzikomo munalibe mwini bwalo wakuchititsa manyazi m'chinthu chilichonse; nasiyana kutali ndi Asidoni, ndipo analibe kanthu ndi munthu aliyense.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthu asanuwo ananyamuka ndipo anafika ku Laisi, kumene anaona kuti anthu ankakhala mwabata monga anthu a ku Sidoni. Anali anthu opanda chowavuta ndiponso aphee. Tsono popeza mʼdziko mwawo analibe chosowa, iwo anali a chuma. Anaonanso kuti anthuwo ankakhala kutali ndi Sidoni ndipo analibe ubale ndi wina aliyense.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo amuna asanuwa anacoka, nafika ku Laisi; naona anthu anali m'mwemo, kuti anakhalaokhazikika mtima, monga anakhala Asidoni, odekha ndi osatekeseka; popeza m'dzikomo munalibe mwini bwalo wakudtitsa manyazi m'cinthu ciri conse; nasiyana kutali ndi Asidoni, ndipo analibe kanthu ndi munthu ali yense.