Judges 18:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Okazonda dziko aja atabwerera kwa abale ao ku Zora ndi ku Esitaoli, abale aowo adaŵafunsa kuti, “Nanga mutisimbira zotani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo asanuwo anafikanso kwa abale ao ku Zora ndi Esitaoli; ndi abale ao ananena nao, Mutani inu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ozonda dziko aja atabwerera kwa abale awo ku Zora ndi Esitaoli, abale awowo anawafunsa kuti, “Mwaonako zotani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo asanuwo anafikanso kwa abale ao ku Zora ndi Esitaoli; ndi abale ao ananena nao, Mutani inu?