Judges 18:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adayankha kuti, “Fulumirani, tiyeni tikamenyane nawo nkhondo, pakuti dziko laolo taliwona, nlachonde kwambiri. Monga inu simuchitapo kanthu? Musachedwe kukaloŵa m'dzikomo ndi kukalilanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iwo, Taukani, tiwakwerere; pakuti tapenya dziko, ndipo taonani, ndilo lokoma ndithu; ndi inu muli chete kodi? Musamachita ulesi kumuka ndi kulowa kulandira dzikolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tiyeni tikamenyane nawo nkhondo popeza taliona dziko lawolo kuti ndi lachonde kwambiri. Kodi simuchitapo kanthu? Musachite mphwayi kupita mʼdzikomo ndi kukalilanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iwo, Taukani, tiwakwerere; pakuti tapenya dziko, ndipo taonani, ndilo lokoma ndithu; ndi inu muli cete kodi? musamacita ulesi kumuka ndi kulowa kulandira dzikolo,