Judges 19:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo, pamene ku Israele kunalibe mfumu, munthu wina wachilevi ankakhala kutali ku dziko lamapiri la ku Efuremu. Iyeyo adakwatira mzikazi wa ku Betelehemu m'dziko la Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, masiku aja, pamene panalibe mfumu m'Israele, panali munthu Mlevi wogonera kuseri kwa mapiri a Efuremu amene anadzitengera mkazi wamng'ono wa ku Betelehemu-Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyo ku Israeli kunalibe mfumu. Mlevi wina ankakhala kutali ku dziko lamapiri la Efereimu. Iyeyu anatenga mzikazi wa ku Betelehemu, mʼdziko la Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, masiku aja, pamene panalibe mfumu m'Israyeli, panali munthu Mlevi wogonera kutseri kwa mapiri a Efraimu amene anadzitengera mkazi wamng'ono wa ku Betelehemu-Yuda.