Judges 19:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu uja sadafune kugonanso tsiku limenelo. Mwakuti adanyamuka nkumapita, nakafika ku malo oyang'anana ndi Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu). Iyeyo anali atatenga abulu aŵiri okhala ndi zishalo zake, ndipo mzikazi wake uja anali naye limodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma munthuyo anakana kugonako usiku, nanyamuka, nachoka, nadza pandunji pa Yebusi (ndiwo Yerusalemu); ndi pamodzi naye panali abulu awiri omangirira mbereko; anali nayenso mkazi wake wamng'ono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma munthuyo sanafune kugonanso tsiku limenelo. Choncho ananyamuka kumapita, ndipo anakafika ku malo oyangʼanana ndi Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu). Iyeyo anali atatenga abulu ake awiri okhala ndi zokhalira zake, ndipo mzikazi wake uja anali naye limodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma munthuyo anakana kugonako usiku, nanyamuka, nacoka, nadza pandunji pa Yebusi (ndiwo Yerusalemu); ndi pamodzi naye panali aburu awiri omangirira mbereko; anali nayenso mkazi wace wamng'ono.