Judges 19:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapatukira kumeneko kuti akaloŵe mu mzinda wa Gibea, ndi kugona komweko usiku umenewo. Adakaloŵa mumzindamo nakakhala pansi pa bwalo, pakuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe amene adaŵalandira kunyumba kwake, kuti apeze pogona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napatukirako, kuti alowe nagone ku Gibea; nalowa iye, nakhala pansi m'khwalala la mudziwo, pakuti panalibe wina wowalandira m'nyumba agonemo, wakuwapatsa pogona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anapatukira kumeneko kuti alowe mu mzinda wa Gibeya kukagona usiku umenewo. Anakalowa mu mzindamo ndi kukakhala pabwalo popeza panalibe munthu amene anawalandira ku nyumba kwake kuti akagone.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napambukirako, kuti alowe nagone ku Gibeya; nalowa iye, nakhala pansi m'khwalala la mudziwo, pakuti panalibe wina wowalandira m'nyumba agonemo, wakuwapatsa pogona.