Judges 19:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adangoona munthu wina wokalamba akuchokera ku ntchito kumunda kwake madzulo. Anali wa ku dziko lamapiri la ku Efuremu, koma ankakhala nao ku Gibea. (Eni ake malowo anali Abenjamini).
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, munthu nkhalamba anachokera ku ntchito yake kumunda madzulo; munthuyu ndiye wa ku mapiri a Efuremu, nagonera ku Gibea; koma anthu pamenepo ndiwo Abenjamini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake anangoona munthu wina wokalamba akuchokera ku ntchito ya ku munda kwake madzulo. Iyeyu anali wa ku dziko la mapiri ku Efereimu, koma ankakhala ku Gibeya. Koma anthu a kumeneko anali a fuko la Benjamini.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, munthu nkhalamba anacokera ku nchito yace kumunda madzulo; munthuyu ndiye wa ku mapiri a Efraimu, nagonera ku Gibeya; kuma anthu pamenepo ndiwo Abenjamini.