Judges 19:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wokalamba uja atakweza maso adaona wapaulendo uja atakhala pa bwalo la mumzindamo, namufunsa kuti, “Kodi ulendowu, mukupita kuti? Nanga mukuchokera kuti?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene anakweza maso ake anaona munthu wa pa ulendoyo m'khwalala la mudzi; ndi nkhalambayo inati, Umuka kuti? Ufumira kuti?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wokalamba uja anakweza maso ndipo anaona munthu wa paulendo uja atakhala pabwalo la mzindawo, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukupita kuti? Nanga mukuchokera kuti?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene anakweza maso ace anaona munthu wa pa ulendoyo m'khwalala la mudzi; ndi nkhalambayo inati, Umuka kuti? ufumira kuti?