Judges 19:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mlendoyo adayankha kuti, “Tikupita kutali ku dziko lamapiri la ku Efuremu kumene ndimakhala, ndipo tikuchokera ku Betelehemu ku dziko la Yuda. Ndidaapita ku Betelehemu ndipo tsopano ndikupita kwathu, koma palibe ndi mmodzi yemwe wondilandira m'nyumba mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena nayo, Tili kuchokera ku Betelehemu-Yuda, kunka ku mbali za mapiri a Efuremu, ndiko ndifumira ine; koma ndidamuka ku Betelehemu-Yuda; ndipo tsopano ndili kumuka kunyumba ya Yehova; koma palibe munthu wondipatsa nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Tikuchokera ku Betelehemu ku dziko la Yuda ndipo tikupita kutali ku dziko lamapiri la Efereimu kumene ndimakhala. Ndinapita ku Betelehemu mʼdziko la Yuda ndipo tsopano ndikubwerera kwathu. Koma palibe aliyense amene wanditengera ku nyumba yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena nayo, Tirikucokera ku BetelehemuYuda, kumka ku mbali za mapiri a Efraimu, ndiko ndifumira ine; koma ndidamuka ku Betelehemu-Yuda; ndipo tsopano ndiri kumuka ku nyumba ya Yehova; koma palibe munthu wondipatsa nyumba.