Judges 19:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina mzikazi wake uja adamkwiyira mwamunayo ndipo adathaŵa napita kwa bambo wake ku Betelehemu m'dziko la Yuda. Adakhala kumeneko miyezi inai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mkazi wake wamng'ono anachita chigololo akali naye, namchokera kunka kunyumba ya atate wake ku Betelehemu-Yuda, nakhalako nthawi ya miyezi inai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina mzikazi uja anakwiyira mwamuna wake ndipo anamuchokera kupita kwa abambo ake ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Anakakhala kumeneko miyezi inayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mkazi wace wamng'ono anacita cigololo akali naye, namcokera kumka ku nyumba ya atate wace ku Betelehemu-Yuda, nakhalako nthawi ya miyezi inai.