Judges 19:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene anali kudya mosangalala, adangoona anthu amumzindamo, anthu achabechabe, ataizinga nyumbayo, namamenya chitseko. Adauza munthu wokalamba uja, mwini wake wa nyumbayo, kuti, “Mtulutse munthu uja wabwera m'nyumba mwakoyu, tiseŵere naye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pokondweretsa iwo mitima yao, taonani amuna a m'mudziwo, ndiwo anthu otama zopanda pake, anazinga nyumba, nagogodagogoda pachitseko; nati kwa mwini nyumba nkhalambayo ndi kuti, Tulutsa mwamunayo adalowa m'nyumba mwako kuti timdziwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ankadya mosangalala, anangoona anthu ena achabechabe a mu mzindawo azungulira nyumba ija nʼkumamenya chitseko. Tsono anawuza mwini nyumbayo, munthu wokalamba uja kuti, “Mutulutse munthu amene wabwera mʼnyumba yakoyu kuti tigone naye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pokondweretsa iwo mitima yao, taonani amuna a m'mudziwo, ndiwo anthu otama zopanda pace, anazinga nyumba, nagogodagogoda pacitseko; nati kwa mwini nyumba nkhalambayo ndi kuti, Turutsa mwamunayo adalowa m'nyumba mwako kuti timdziwe.