Judges 19:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwini wake wa nyumba uja adatuluka nakaŵauza kuti, “Iyai, abale anga, musachite zoipa zotere. Munthuyu wabwera m'nyumba mwanga muno, musachite chinthu chonyansa chotere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu mwini nyumba anawatulukira nanena nao, Iai, abale anga, musachite choipa chotere; popeza mwamuna uyu walowa m'nyumba mwanga, musachite chopusa ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mwini nyumba uja anatuluka ku bwalo nawawuza kuti, “Ayi, abale anga musachite zoyipa zotere. Popeza munthu uyu walowa mʼnyumba mwanga muno, musachite chinthu chonyansa chotere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu mwini nyumba anawaturukira nanena nao, lai, abale anga, musacite coipa cotere; popeza mwamuna uyu walowa m'nyumba mwanga, musacite copusa ici.