Judges 19:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani pano pali mwana wanga wanamwali wosamdziŵa mwamuna pamodzi ndi mzikazi wa mlendoyu. Ndikutulutsireni ameneŵa tsopano lino, muŵatenge ndipo muchite nawo zimene mufuna. Koma musachite chinthu chonyansa ndi mlendoyu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, mwana wanga wamkazi ndiye namwali, ndi mkazi wake wamng'ono siwa; ndiwatulutse iwo, muwachepetse iwo, ndi kuwachitira monga muyesa chokoma; koma mwamuna uyu musamchitire chopusa ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onani, pano pali mwana wanga wamkazi wosadziwa mwamuna pamodzi ndi mzikazi wa mlendoyu. Ndikutulutsirani amenewa tsopano ndipo atengeni ndi kuchita nawo chomwe chikukomerani. Koma musachite chinthu chonyansa ndi munthuyu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, mwana wanga wamkazi ndiye namwali, ndi mkazi wace wamng'onoyo siwa; ndiwaturutse iwo, muwacepetse iwo, ndi kuwacitira monga muyesa cokoma; koma mwamuna uyu musamcitire copusa ici.