Judges 19:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthuwo sadafune kumumvera. Choncho mlendo uja adagwira mzikazi wake uja namtulutsira kunali iwoko, iwowo nkugona naye, nachita naye zoipa usiku wonse mpaka m'maŵa. M'bandakucha adamlola kuti apite.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma amunawo sanafune kumvera; motero munthuyu anagwira mkazi wake wamng'ono, natuluka naye kwa iwo kunja; namdziwa iwo, nachita naye zoipa usiku wonse mpaka m'mawa; namlola achoke mbandakucha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthuwo sanafune kumumvera. Choncho mlendo uja anagwira mzikazi wake namutulutsa kuja kumene kunali iwo. Tsono iwowo anagona naye ndi kuchita naye zonyansa usiku wonse mpaka mmawa. Mʼbandakucha anamulola kuti apite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma amunawo sanafuna kumvera; motero munthuyu anagwira mkazi wace wamng'ono, naturuka naye kwa iwo kunja; namdziwa iwo, nacita naye zoipa usiku wonse mpaka m'mawa; namlola acoke mbandakuca.