Judges 19:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwamuna wakeyo adadzuka m'maŵa, ndipo atatsekula zitseko za nyumba kuti azipita, anangoona mzikazi wake uja ali thasa pakhomo pa nyumba, manja ake ali pa chiwundo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene mbuye wake anauka mamawa, natsegula pakhomo pa nyumba, natuluka kunka ulendo wake, taona, mkazi wake wamng'ono, atagwa pakhomo pa nyumba ndi manja ake pachiundo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwamuna wake anadzuka mʼmamawa, natsekula chitseko cha nyumba kuti atuluke ndi kumapita. Koma anangoona mzikazi wake uja ali thapsa pa khomo la nyumbayo, manja ake ali pa khonde.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene mbuye wace anauka mamawa, natsegula pakhomo pa nyumba, naturuka kumka ulendo wace, taona, mkazi wace wamng'onoyo, atagwa pakhomo pa nyumba ndi manja ace paciundo.