Judges 19:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamuuza kuti, “Dzuka tizipita.” Koma mkaziyo sadayankhe kanthu. Tsono adamkweza pabulu, ndipo mlendoyo adanyamuka kupita kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena naye, Tauka, timuke; koma panalibe womyankha. Pamenepo anamuika pa bulu; nanyamuka mwamunayo, namka kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati kwa mkaziyo, “Dzuka tizipita.” Koma sanayankhe kanthu. Kenaka anamukweza pa bulu wake ndipo ananyamuka kumapita kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena naye, Tauka, timuke; koma panalibe womyankha. Pamenepo anamuika pa buru; nanyamuka mwamunayo, namka kwao.