Judges 19:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ataloŵa m'nyumba mwake, adatenga mpeni, naduladula thupi la mkaziyo m'nthuli khumi ndi ziŵiri. Ndipo adazitumiza m'dziko lonse la Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofika iye kunyumba kwake, anatenga mpeni, nagwira mkazi wake wamng'onoyo namgawa chiwalochiwalo magawo khumi ndi awiri, namtumiza ku malire onse a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika ku nyumba yake, anatenga mpeni, nagwira mzikazi wake uja ndi kuduladula thupi lake nthuli khumi ndi ziwiri. Kenaka anazitumiza ku zigawo zonse za Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pofika iye kunyumba kwace, anatenga mpeni, nagwira mkazi wace wamng'onoyo namgawa ciwalo ciwalo magawo khumi ndi awiri, namtumiza ku mame onse a Israyeli.