Judges 19:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mwamuna wake adanyamuka namtsatira kuti akakambe naye mofatsa, kumpempha kuti abwerere. Mwamunayo anali ndi mtumiki wake ndi abulu ake aŵiri. Ndipo adafika ku nyumba ya bambo wake wa mkaziyo. Tsono mkaziyo adamloŵetsa m'nyumba ndipo bambo wake adamlandira ndi manja aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anauka mwamuna wake namtsata kukamba naye zamtima, kumbwezanso; napita ndi mnyamata wake, ndi abulu awiri. Ndipo mkaziyo anadza naye kunyumba ya atate wake. Ndipo pakumuona atate wa mkaziyo anakondwera kukomana naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwamuna wake anamulondola kuti akayankhule naye mofatsa kumupempha kuti abwerere. Iye anali ndi antchito ake ndi abulu ake awiri. Anafika ku nyumba kwa mkazi uja ndipo iye anamulowetsa mʼnyumba ya abambo ake. Abambo aja atamuona mnyamata uja anamulandira mwachimwemwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anauka mwamuna wace namtsata kukamba naye zamtima, kumbwezanso; napita ndi mnyamata wace, ndi aburu awiri. Ndipo mkaziyo anadza naye ku nyumba ya atate wace. Ndipo pakumuona atate wa mkaziyo, anakondwera kukomana naye.