Judges 19:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse amene adaona zimenezi ankati, “Zoterezi sizinachitikepo kuyambira nthaŵi imene Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito mpaka lero lino. Tiziganize bwino ndipo tipangane ndi kuchitapo kanthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali kuti onse amene anachiona anati, Sichinachitika, inde sichinaoneka chotere chiyambire tsiku lokwera ana a Israele kutuluka m'dziko la Ejipito mpaka lero lino; lingiriranipo, mupangane nzeru, nimunene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene anaona zimenezi ankanena kuti, “Zoterezi sizinaonekepo kuyambira pamene Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ganizirani bwino chinthu chimenechi ndipo tiwuzeni zoyenera kuchita!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali kuti onse amene anaciona anati, Sicinacitika, inde sicinaoneka cotere ciyambire tsiku lokwera ana a Israyeli kuturuka m'dziko la Aigupto mpaka lero lino; lingiriranipo, mupangane nzeru, nimunene.