Judges 19:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lachinai lake iwo adadzuka m'mamaŵa, iye nkukonzeka kuti azipita. Koma bambo wake wa mkaziyo adauza mkamwini wake uja kuti, “Yambani mwadya chakudya, pambuyo pake mutha kupita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, tsiku lachinai, analawirira mamawa, nanyamuka iye kuchoka; koma atate wa mkaziyo anati kwa mkamwini wake, Limbitsa mtima wako ndi mkate pang'ono, ndipo utatero upite.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lachinayi anadzuka mʼmamawa kukonzekera kuti azipita kwawo, koma abambo ake a mtsikanayo anawuza mkamwini wawo uja kuti, “Yambani mwadya chakudya, ndipo kenaka mutha kupita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, tsiku lacinai, analawirira mamawa, nanyamuka iye kucoka; koma atate wa mkaziyo anati kwa mkamwini wace, Limbitsa mtima wako ndi mkate pang'ono, ndipo utatero upite.