Judges 19:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho anthu aŵiriwo adakhala pansi, nadya ndi kumwa limodzi. Bambo wa mkaziyo adauza mwamunayo kuti, “Gonaninso konkuno lero, musangalale.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nakhala pansi nadya namwa onse awiri pamodzi; nati kwa munthuyo atate wa mkaziyo, Uvomere, ugone kuno usiku, nusekerere mtima wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho onse awiri anakhala pansi ndi kudya ndi kumwa pamodzi. Atadya, abambo a mtsikanayo anati, “Chonde mugonenso konkuno musangalale.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nakhala pansi nadya namwa onse awiri pamodzi; nati kwa munthuyo atate wa mkaziyo, Ubvomere, ugone kuno usiku, nusekerere mtima wako.