Judges 19:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lachisanu lake adadzuka m'mamaŵa kuti azipita. Bambo wake wa mkaziyo adamuuza kuti, “Yambani mwadya chakudya ndipo mudikire mpaka madzulo.” Choncho aŵiri onsewo adadyera limodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nalawirira mamawa tsiku lachisanu kuti amuke, koma atate wa mkaziyo anati, Ulimbitse mtima wako, nulindire lipendeke dzuwa; nadya iwo onse awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa wa tsiku lachisanu, atadzuka kuti azipita abambo ake a mtsikanayo anamuwuza kuti, “Yambani mwadya chakudya ndipo mutandale mpaka madzulo.” Choncho awiriwo anadya pamodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nalawirira mamawa tsiku lacisanu kuti amuke, koma atate wa mkaziyo anati, Ulimbitse mtima wako, nulindire lipendeke dzuwa; nadya iwo onse awiri.