Judges 19:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene munthuyo ndi mzikazi wake ndiponso mtumiki wake adanyamuka kuti azipita, bambo wake wa mkaziyo adaŵauza kuti, “Onani, dzuŵa ndiye lapita, ndipo ano ndi madzulo. Gonaninso konkuno lero ndapota nanu. Onani kulikuda. Gonani konkuno, musangalale. Maŵa mudzuka m'mamaŵa nkumapita kwanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo munthuyo ananyamuka kuchoka, iye ndi mkazi wake wamng'ono ndi mnyamata wake; koma mpongozi wake, atate wa mkaziyo, ananena naye, Tapenya, lapendeka dzuwa, ugone kuno usiku; tapenya lapendekatu dzuwa, ugone kuno, nusekerere mtima wako; nimulawire mamawa kunka ulendo wanu kwanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake munthu uja pamodzi ndi mzikazi wake ndiponso mtumiki anakonzeka kuti azipita. Koma abambo a mtsikana uja anatinso kwa iye, “Onani tsopano kukuda. Gonani konkuno pakuti tsiku latha kale. Gonani ndipo musangalale. Mawa mudzuka mʼmamawa ndi kumapita kwanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo munthuyo ananyamuka kucoka, iye ndi mkazi wace wamng'ono ndi mnyamata wace; koma mpongozi wace, atate wa mkaziyo, ananena naye, Tapenya, lapendeka dzuwa, ugone kuno usiku; tapenya lapendekatu dzuwa, ugone kuno, nusekerere mtima wako; nimulawire mamawa kumka ulendo wanu kwanu.