Judges 2:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngelo wa Chauta adapita ku Bokimu kuchokera ku Giligala. Ndipo adauza Aisraele kuti, “Ndidakutulutsani ku Ejipito ndi kukuloŵetsani m'dziko limene ndidalumbira kuti ndidzapatsa makolo anu. Ndidati, ‘Ineyo sindidzaswa konse chipangano changa ndi inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kuchokera ku Giligala kunka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kuchokera ku Ejipito, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola chipangano changa nanu ku nthawi yonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wa Yehova anapita ku Bokimu kuchokera ku Giligala ndipo anati kwa Aisraeli, “Ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndikukulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira kwa makolo anu. Ndinati ‘Sindidzaswa pangano langa ndi inu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kucokera ku Giligala kumka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kucokera ku Aigupto, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola cipangano canga nanu ku nthawi yonse;