Judges 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao, amene adaŵatulutsa m'dziko la Aejipito. Adatsata milungu ina ya anthu oŵazungulira, ndipo ankaipembedza. Pakutero adakwiyitsa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawatulutsa m'dziko la Ejipito, natsata milungu ina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa ku Igupto. Ndipo anatsatira ndi kupembedza milungu yosiyanasiyana ya anthu amene anawazungulira. Motero Aisraeli anakwiyitsa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawaturutsa m'dziko la Aigupto, natsata milungu yina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova.