Judges 2:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Chauta adaŵapsera mtima Aisraelewo, ndipo adaŵapereka m'manja mwa anthu ofunkha amene adasakaza zinthu zao. Ndipo adalola kuti adani ao oŵazungulira aŵagonjetse, kotero kuti sadathenso kulimbana nawo adaniwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha amene ankasakaza zinthu zawo. Ndipo analola kuti adani awo owazungulira amene sanathenso kulimbana nawo, awagonjetse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.