Judges 2:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankati akapita kukamenya nkhondo, Chauta ankalimbana nawo iwowo, monga momwe Iye adaanenera molumbira kuti adzaterodi. Choncho Aisraelewo anali pa mavuto oopsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuli konse anatuluka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi zonse Aisraeli ankati akapita ku nkhondo, Yehova amalimbana nawo kuti agonjetsedwe, monga ananenera molumbira kuti zidzaterodi. Choncho iwo anali pa mavuto aakulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuli konse anaturuka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa.