Judges 2:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi zonse Chauta akaŵautsira mtsogoleri, Chauta ankakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankaŵapulumutsa Aisraele kwa adani ao nthaŵi zonse mtsogoleriyo ali moyo. Zoonadi Chauta ankaŵamvera chisoni anthuwo, iwowo akamamdandaulira chifukwa cha amene ankaŵazunza ndi kuŵasautsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi zonse Yehova akawautsira mtsogoleri, Iye amakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankawapulumutsa Aisraeliwo mʼmanja mwa adani awo mʼnthawi imene anali moyo. Yehova ankawamvera chisoni Aisraeli pamene ankabuwula chifukwa cha anthu owazunza ndi kuwasautsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa cisoni pa kubuula kwao cifukwa ca iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.