Judges 2:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Chauta adaŵapsera mtima Aisraele, nati, “Anthuŵa aphwanya chipangano changa chimene ndidaakhazikitsira makolo ao. Ndiye popeza kuti sadamvere mau anga,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele; nati Iye, Popeza mtundu uwu unalakwira chipangano changa chimene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau anga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeli ndipo anati, “Chifukwa mtundu uwu waswa pangano limene ndinakhazikitsa ndi makolo awo ndipo sanandimvere,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli; nati Iye, Popezamtundu uwu unalakwira cipangano canga cunene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau ansa;