Judges 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho tsopano ndikukuuzani kuti sindidzapirikitsa nzikazo pamene inu mukufika. Koma zidzasanduka adani anu, ndipo milungu yao idzakhala ngati msampha kwa inu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chakenso ndinati, Sindidzawapirikitsa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m'nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikukuwuzani tsopano kuti sindithamangitsa nzikazo pamene inu mukufika. Ndidzawasandutsa kukhala adani anu ndipo milungu yawo idzakhala ngati msampha kwa inu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cacenso ndinati, Sindidzawapitikitsa kuwacotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m'nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha.