Judges 2:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo ankatumikira Chauta masiku onse pamene Yoswa anali moyo, ndipo ngakhale atafa Yoswayo, anthu ankatumikirabe Chauta nthaŵi yonse ya moyo wa akuluakulu otsatira Yoswa aja, amene anali ataona ntchito zazikulu zimene Chauta adachitira Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene adaona ntchito yaikulu yonse ya Yehova anaichitira Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a moyo wa Yoswa. Atamwalira Yoswa, Aisraeli anatumikirabe Yehova nthawi yonse ya moyo wa akuluakulu amene anaona zazikulu zimene Yehova anawachitira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa ndi masiku onse a akulu akulu otsala atafa Yoswa, amene adaona nchito yaikuru yonse ya Yehova anaicitira Israyeli.