Judges 20:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'mafuko onse a Aisraele tisankhula anthu khumi pa anthu 100 aliwonse. Ameneŵa adzasonkhanitsa zakudya za ankhondo, ndipo ankhondowo adzapita kukalipsira anthu a ku Gibea, mzinda wa ku Benjamini, chifukwa cha tchimo lao lonyansa zedi limene adachita m'dziko la Israele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tidzatapa amuna khumi limodzi pa zana limodzi, mwa mafuko onse a Israele; ndi zana limodzi pa zikwi chimodzi, ndi chikwi chimodzi pa zikwi khumi kutengera anthu kamba; kuti pakufika ku Gibea wa Benjamini, auchitire monga mwa chopusa chonse unachita m'Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmafuko onse a Aisraeli tidzasankha anthu khumi pa anthu 100 aliwonse: ndiye kuti anthu 100 pa anthu 1,000 aliwonse kapena anthu 1,000 pa anthu 10,000 aliwonse. Anthu amenewa adzasonkhanitsa zakudya za ankhondo, ndipo ankhondowo adzapita kukalipsira anthu a ku Geba mʼdziko la Benjamini chifukwa chochita chinthu chonyansa chotere mʼdziko la Israeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tidzatapa amuna khumi limodzi pa zana limodzi, mwa mapfuko onse a Israyeli; ndi zana limodzi pa zikwi cimodzi, ndi cikwi cimodzi pa zikwi khumi kutengera anthu kamba; kuti pakufika ku Gibeya wa Benjamini, aucitire monga mwa copusa conse unacita m'Israyeli.